Cifukwa ca zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi:Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditarikira;Ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.