Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 1:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ha! mudziwo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha!Ukunga mkazi wamasiye!Waukuruwo mwa amitundu, kalonga wamkazi m'madera a dzikoWasanduka wolamba!

2. Uliralira usiku; misozi yace iri pa masaya ace;Mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza:Mabwenzi ace onse aucitira ziwembu,Asanduka adani ace.

3. Yuda watengedwa ndende cifukwa ca msauko ndi ukapolo waukuru;Akhala mwa amitundu, sapeza popuma;Onse akumlondola anampeza pakati popsinjikiza.

4. M'njira za Ziyoni mulira posoweka akudzera msonkhano;Pa zipata zace zonse papasuka; ansembe ace onse ausa moyo;Anamwali ace asautsidwa; iye mwini namva zowawa.

5. Amaliwongo ace asanduka akuru ace, adani ace napindula;Pakuti Yehova wamsautsa pocuruka zolakwa zace;Ana ace ang'ono alowa m'ndende pamaso pa adani ace.

6. Ulemu wace wonse wamcokera mwana wamkazi wa Ziyoni;Akalonga ace asanduka nswala zosapeza busa,Anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompitikitsa.

7. M'masiku a msauko wace ndi kusocera kwaceYerusalemu ukumbukira zokondweretsa zace zonse zacikhalire;Pogwidwa anthu ace ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa,Adaniwo anamuona naseka mwacipongwe mabwinja ace.

8. Yerusalemu wacimwa kwambiri; cifukwa cace wasanduka cinthu conyansa;Onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamarisece;Inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.

9. Udio wace unali m'nsaru zace; sunakumbukira citsiriziro cace;Cifukwa cace watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza;Taonani Yehova, msauko wanga, pakuti mdaniyo wadzikuzayekha.

10. Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zace zonse;Pakuti waona amitundu atalowa m'malo ace opatulika,Amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.

Werengani mutu wathunthu Maliro 1