Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Malaki 1:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. KATUNDU wa mau a Yehova wa kwa Israyeli mwa Malaki.

2. Ndakukondani, ati Yehova; koma inu mukuti, Mwatikonda motani? Esau si mkulu wace wa Yakobo kodi? ati Yehova; ndipo ndinakonda Yakobo;

3. koma Esau ndinamuda, ndinasanduliza mapiri ace abwinja, ndi kupereka colowa cace kwa ankhandwe a m'cipululu.

4. Cinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawacha, Dziko la coipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao cikwiyire.

5. Ndipo maso anu adzaona, nimudzati, Yehova ali wamkuru kupitirira malire a Israyeli.

6. Mwana alemekeza atate wace, ndi mnyamata mbuye wace; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?

7. Mupereka mkate wodetsedwa pa guwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M'menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka.

8. Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe coipa! ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe coipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? kapena adzakubvomerezani kodi? ati Yehova wa makamu.

9. Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti aticitire cifundo; icico cicokera kwa inu; kodi Iye adzabvomereza ena a inu? ati Yehova wa makamu.

Werengani mutu wathunthu Malaki 1