Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 6:25-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Lankhula ndi Aroni ndi ana ace, ndi kuti, Cilamulo ca nsembe yaucimo ndi ici: Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo pophera nsembe yaucimo pamaso pa Yehova; ndiyo yopatulikitsa.

26. Ndipo azidya iyi wansembe amene aipereka cifukwa ca zoipa; aidyere m'malo opatulika, pa bwalo la cihema cokomanako.

27. Ali yense akakhudza nyama yace adzakhala wopatulika; ndipo akawaza mwazi wace wina pa cobvala ciri conse, utsuke cimene adauwazaco m'malo opatulika.

28. Ndipo mphika wadothi umene anaphikamo nyamayi auswe, koma ngati anaiphika mu mphika wamkuwa, atsuke uwu, nautsukuluze ndi madzi.

29. Amuna onse a mwa ansembe adyeko; ndiyo yopatulikitsa.

30. Koma asadye nsembe yaucimo iri yonse, imene amadza nao mwazi wace ku cihema cokomanako kutetezera nao m'malo opatulika; aitenthe ndi moto.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 6