Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 6:14-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo cilamulo ca copereka caufa ndico: ana a Aroni azibwera naco pamaso pa Yehova ku guwa la nsembe.

15. Ndipo atengeko wodzala manja pa ufa wa copereka ca ufa wosalala, ndi pa mafuta ace, ndi libona lonse liri pa copereka caufa, nazitenthe pa guwa la nsembe, zicite pfungo lokoma, ndizo cikumbutso cace ca kwa Yehova.

16. Ndipo cotsalira cace adye Aroni ndi ana ace; acidye copanda cotupitsa m'malo opatulika; pa bwalo la cihema cokomanako acidye.

17. Asaciphike ndi cotupitsa, Ndacipereka cikhale gawo lao locokera pa nsembe zanga zamoto; ndico copatulikitsa, monga nsembe yaucimo, ndi monga nsembe yoparamula.

18. Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, ciwacokere ku nsembe zamoto za Yehova; ali yense wakuzikhudza izi adzakhala wapatolika.

19. Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,

20. Copereka ca Aroni ndi ana ace, cimene azibwera naco kwa Yehova tsiku la kudzozedwa iye ndi ici: limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale copereka caufa kosalekeza, nusu lace m'mawa, nusu lace madzulo.

21. Cikonzeke paciwaya ndi mafuta; udze naco cokazinga; copereka caufa cazidutsu ubwere naco, cikhale pfungo lokoma la kwa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 6