Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 6:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2. Akacimwa munthu nakacita mosakhulupirika pa Yehova nakacita monyenga ndi mnansi wace kunenaza coikiza, kapena cikole, kapena cifwamba, kapena anasautsa mnansi wace;

3. kapena anapeza cinthu cotayika, nanenapo bodza, nalumbira pabodza; pa cimodzi ca izi zonse amacita munthu, ndi kucimwapo;

4. pamenepo padzali kuti popeza anacimwa, naparamula, azibweza zofunkha zimene analanda mwacifwamba, kapena cinthuci adaciona ndi kusautsa mnzace, kapena coikiza anamuikiza, kapena cinthu cotayika anacipeza;

5. kapena ciri conse analumbirapo monama; acibwezere conseci, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ici kwa mwini wace tsiku lotsutsidwa iye.

6. Ndipo adze nayo nsembe yace yoparamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda cirema ya m'khola mwace, monga umayesa mtengo wace, ikhale nsembe yoparamula, adze nayo kwa wansembe;

7. ndipo wansembeyo amcitire comtetezera pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa; kunena ziti zonse akazicita ndi kuparamula nazo.

8. Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,

9. Uza Aroni ndi ana ace, ndi kuti, Cilamulo ca nsembe yopsereza ndi ici: nsembe yopsereza izikhala pa nkhuni za pa guwa la nsembe usiku wonse kufikira m'mawa; ndipo mota wa pa guwa la nsembe uziyakabe pamenepo.

10. Ndipo wansembe abvale mwinjiro wace wabafuta, nabvale pathupi pace zobvala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, mota utanyeketsa nsembe yamoto pa guwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe.

11. Pamenepo abvule zobvala zace, nabvale zobvala zina, nacotse phulusa kumka nalo kunja kwa cigono, kumalo koyera.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 6