Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 27:2-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Nena ndi ana a Israyeli, nuti nao, Pamene munthu acita cowinda ca padera, anthuwo azikhala a Yehova monga mwa kuyesa kwako.

3. Ukayesa wamwamuna wa zaka makumi awiri kufikira wina wa zaka makumi asanu ndi limodzi, uziwayesera a masekeli makumi asanu a siliva, monga mwa sekeli wa malo opatulika.

4. Koma akakhala wamkazi, umuyesere wa masekeli makumi atatu.

5. Akakhala munthu wa zaka zisanu kufikira wina wa zaka makumi awiri uwayesere, wamwamuna wa masekeli makumi awiri, ndi wamkazi wa masekeli khumi.

6. Akakhala mwana wa mwezi umodzi kufikira zaka zisanu, uziwayesera wamwamuna wa masekeli asanu a siliva, ndi wamkazi wa masekeli atatu a siliva.

7. Akakhala munthu wa zaka makumi asanu ndi limodzi ndi mphambu, akakhala wamwamuna, umuyesere wa masekeli khumi ndi asanu, akakhala wamkazi wa masekeli khumi.

8. Koma cuma cace cikapanda kufikira kuyesa kwako, amuike pamaso pa wansembe, kuti wansembeyo amuyese; ndipo wansembeyo amuyese, monga akhoza iye amene anawinda.

9. Ndipo cikakhala ca nyama imene anthu amabwera nayo ikhale copereka ca Yehova, zonse zotere munthu akazipereka kwa Yehova zikhale zopatulika.

10. Asaisinthe, yokoma m'malo mwa yoipa, kapena yoipa m'malo mwa yokoma; ndipo akasinthadi nyama m'malo mwa inzace, pamenepo iyo ndi yosinthikayo zikhale zopatulika.

11. Ndipo cikakhala ca nyama yodetsa, imene sabwera nayo ikhale copereka ca Yehova, aike nyamayi pamaso pa wansembe;

12. ndipo wansembeyo aiyese mtengo wace, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga uiyesa wansembewe, momwemo.

13. Ndipo akaiombola ndithu, pamenepo aonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wace.

14. Munthu akapatula nyumba yace ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe aziiyesa mtengo wace, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga wansembeyo aiyesa, ikhale momwemo.

15. Ndipo iye wakuipatula akaombola nyumba yace, aonjezepo limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo idzakhala yace.

16. Munthu akapatulirako Yehova munda wace wace, uziuyesa monga mwa mbeu zace zikakhala; homeri wa barie uuyese wa masekeli makumi asanu a siliva.

17. Akapatula munda wace kuyambira caka coliza lipenga, mundawo ukhale monga momwe unauyesera.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 27