Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 26:30-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

30. Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu.

31. Ndipo ndidzasandutsa midzi yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za pfungo lanu lokoma.

32. Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m'mwemo adzadabwa nako.

33. Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi midzi yanu idzakhala bwinja.

34. Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ace, masiku onse a kupasuka kwace, pokhala inu m'dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ace.

35. Masiku onse a kupasuka kwace lipumula; ndiko mpumulo udalisowa m'masabata anu, pokhala inu pamenepo.

36. Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapitikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.

37. Ndipo adzakhumudwitsana monga pothawa lupanga, wopanda wakuwalondola; ndipo mudzakhala opanda mphamvu yakuima pamaso pa adani anu.

38. Ndipo mudzatayika mwa amitundu, ndi dziko la adani anu lidzakudyani.

39. Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m'moyo ndi mphulupulu zao m'maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m'moyo.

40. Pamenepo adzabvomereza mphulupulu zao, ndi mphulupulu za makolo ao, pocita zosakhulupirika pa Ine; ndiponso popeza anayenda motsutsana ndi Ine,

41. Inenso ndinayenda motsutsana nao, ndi kuwatengera ku dziko la adani ao. Ngati tsono mtima wao wosadulidwa udzicepetsa, ndipo abvomereza kulanga kwa mphulupulu zao;

42. pamenepo ndidzakumbukila pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isake, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukila; ndipo ndidzakumbukila dzikoli.

43. Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ace, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzabvomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga.

44. Ndiponso pali icinso: pokhala iwo m'dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kutyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Muhmgu wao.

45. Koma cifukwa ca iwo ndidzawakumbukila pangano la makolo ao, amene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto pamaso pa amitundu, kuti ndikhale Mulungu wao; Ine ndine Yehova.

46. Awa ndi malemba ndi maweruzo ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa iye ndi ana a Israyeli m'phiri la Sinai, ndi dzanja la Mose.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 26