Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 26:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena coimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umene; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

2. Musunge masabata anga, ndi kucitira ulemu malo anga opatulika; Ine ndine Yehova.

3. Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwacita;

4. ndidzakupatsani mvula m'nyengo zace, ndi dziko lidzapereka zipatso zace, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zace.

5. Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yochera mphesa, ndi nyengo yochera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta naco cakudya canu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika.

6. Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zirombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu.

7. Mudzapitikitsa adani anu, ndipo adzagwa pamaso panu ndi lupanga,

8. Asanu ainu adzapitikitsa zana limodzi, ndi zana limodzi la inu adzapitikitsa zikwi khumi; ndi adani anu adzagwa pamaso panu ndi lupanga.

9. Ndipo ndidzatembenukira kwa inu, ndi kukubalitsani, ndi kukucurukitsani; ndipo ndidzakhazika cipangano canga ndinapangana nanuco.

10. Ndipo mudzadya za sundwe wakale ndi kuturutsa zakale cifukwa ca zatsopano.

11. Ndidzamanga kacisi wanga pakati pa inu, ndipo moyo wanga sudzanyansidwa nanu.

12. Ndipo ndidzayendayenda pakati pa inu, ndi kukhala Mulungu wanu ndi inu mudzakhala anthu anga.

13. Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakuturutsani m'dziko la Aigupto, kuti musakhale akapolo ao; ndipo ndinatyola mitengo ya magoli anu, ndi kukuyendetsani coweramuka.

14. Koma mukapanda kundimvera Ine, osacita malamulo awa onse;

15. ndipo mukakaniza malemba anga, ndi moyo wanu ukanyansidwa nao maweruzo anga, kotero kuti simudzacita malamulo anga onse, koma kutyola cipangano canga;

Werengani mutu wathunthu Levitiko 26