Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 23:35-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

35. Tsiku loyamba likhale msonkhano wopatulika, musamagwira nchito ya masiku ena.

36. Masiku asanu ndi awiri mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; tsiku lacisanu ndi citatu mukhale nao msonkhano wopatulika; ndipo mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; ndilo lotsirizira; musamagwira nchito ya masiku ena.

37. Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, zimene muzilalikira zikhale masonkhano opatulika, kukabwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova, nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, nsembe yophera, ndi nsembe yothira, yonse pa tsiku lace lace;

38. pamodzi ndi masabata a Yehova, ndi pamodzi ndi mphatso zanu, ndi pamodzi ndi zoo winda zanu zonse, ndi pamodzi ndi zopereka zaufulu zanu, zimene muzipereka kwa Yehova.

39. Koma tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi wacisanu ndi ciwiri, mutatuta zipatso za m'dziko, muzisunga madyerero a Yehova masiku asanu ndi awiri; tsiku loyamba mupumule, ndi tsiku lacisanu ndi citatu mupumule.

40. Ndipo tsiku loyambali mudzitengere nthambi za mitengo yokoma, nsomo za kanjedza, ndi nthambi za mitengo yobvalira, ndi misondodzi ya kumtsinje; ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu masiku asanu ndi awiri.

41. Ndipo muwasunge madyerero a Yehova masiku asanu ndi awiri m'caka; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; musunge mwezi wacisanu ndi ciwiri.

42. Mukhale m'misasa masiku asanu ndi awiri; onse obadwa m'dziko mwa Israyeli akhale m'misasa;

43. kuti mibadwo yanu ikadziwe lruti ndinakhalitsa ana a Israyeli m'misasa, pamene ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

44. Ndipo Mose anafotokozera ana a Israyeli nyengo zoikika za Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 23