Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 23:21-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Ndipo mulalikire tsiku lomwelo; kuti mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira nchito ya masiku ena; ndilo lemba losatha m'nyumba zanu zonse, mwa mibadwo yanu yonse.

22. Ndipo pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wako.

23. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

24. Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko cikumbutso ca kuliza malipenga, msonkhano wopatulika.

25. Musamagwira nchito ya masiku ena; mubwere nayo nsembe yamoto ya Yehova.

26. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

27. Komatu, tsiku lakhumi la mwezi uwu wacisanu ndi ciwiri, ndilo tsiku la citetezero; mukhale nao msonkhano wopatulika, ndipo mudzicepetse; ndi kubwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova.

28. Musamagwira nchito iri yonse tsiku limenelo; pakuti ndilo tsiku la citetezero, kucita cotetezera inu pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

29. Pakuti munthu ali yense wosadzicepetsa tsiku limenelo, amsadze kwa anthu a mtundu wace.

30. Ndi munthu ali yense wakugwira nchito iri yonse tsiku limenelo, ndidzaononga munthuyo pakati pa anthu a mtundu wace.

31. Musamagwira nchito iri yonse; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu, m'nyumba zanu zoo nse.

32. Likhale ndi inu Sabata lakupumula; ndipo mudzicepetse; tsiku lacisanu ndi cinai madzulo, kuyambira madzulo kufikira madzulo musunge Sabata lanu.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 23