Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 19:5-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo pamene muphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandiridwe.

6. Tsiku lomwelo mwaipha, ndi m'mawa mwace muidye; ngati katsalirako kanthu tsiku lacitatu, muzikatentha ndi moto.

7. Akakadya konse tsiku tacitatu kali conyansa, kosabvomerezeka:

8. koma ali yense akudyako adzasenza mphulupulu yace, popeza waipsa copatulidwa ca Yehova; ndi munthuyo amsadze, kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.

9. Pakukolola dzinthu za m'dziko mwanu, usamakololetsa m'mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha.

10. Usamakunkha khunkha la m'munda wako wamphesa, usamazitola zidagwazi za m'munda wako wamphesa; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

11. Musamaba, kapena kunyenga, kapena kunamizana.

12. Musamalumbira monama ndi kuchula dzina langa, ungaipse dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

13. Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zace; mphotho yace ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m'mawa.

14. Usamatemberera wogontha; usamaika cokhumudwitsa pamaso pa wosaona; koma uziopa Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

15. Musamacita cisalungamo pakuwemza mlandu; usamabvomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.

16. Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.

17. Usamamuda mbale wako mumtima mwako; umdzudzule munthu mnzako ndithu, usadzitengera ucimo cifukwa ca iye.

18. Usamabwezera cilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; Ine ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 19