Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 19:19-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Muzisunga malemba anga, Usamalola zoweta zako za mitundu yosiyana zikwerane; usamabzala m'munda mwako mbeu za mitundu iwiri; usamabvala cobvala ca nsaru za mitundu iwiri zosokonezana.

20. Munthu akagona ndi mkazi, ndiye mdzakazi, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, wosamuombola kapena wosapatsidwa ufulu, akwapulidwe; asawaphe, popeza si mfulu mkaziyo.

21. Ndipo adze nayo nsembe yace yoparamula kwa Yehova, ku khomo la cihema cokomanako, ndiyo nkhosa yamphongo ikhale nsembe yoparamula.

22. Ndipo wansembe acite comtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yoparamula pamaso pa Yehova, cifukwa ca kucimwa adacimwaku; ndipo adzakhululukidwa cifukwa ca kucimwa kwace adacimwaku.

23. Ndipo mukadzalowa m'dzikomo, ndi kubzalamitengo yamitundumitundu ikhale ya cakudya, muziyese zipatso zao monga kusadulidwa kwao; zaka zitatu muziyese zosadulidwa; zisadyedwa.

24. Koma caka cacinai zipatso zace zonse zikhale zopatulika, za kumlemekeza nazo Yehova.

25. Caka cacisanu muzidya zipatso zace, kuti zobala zace zikucurukireni inu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

26. Musamadya kanthu ndi mwazi wace; musamacita nyanga, kapena kuombeza ula.

27. Musamameta mduliro, kapena kusenga m'mphepete mwa ndebvu zanu,

28. Musamadziceka matupi anu cifukwa ca akufa, kapena kutema mpbini; Ine ndine Yehova.

29. Usamaipsa mwana wako wamkazi ndi kumcititsa cigololo; lingadzale ndi cigololo dzikoli, ndi kudzazidwa nazo zocititsa manyazi.

30. Muzisunga masabata anga, ndi kucitira ulemu malo anga opatulika; Ine ndine Yehova.

31. Musamatembenukira kwa obwebweta, kapena anyanga; musawafuna, ndi kudetsedwa nao; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

32. Pali aimvi uziwagwadira, nucitire ulemu munthu wokalamba; nuope Mulungu wako; lnendine Yehova.

33. Ndipo mlendo akagonera m'dziko mwanu, musamamsautsa.

34. Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m'dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m'dziko la Aigupto; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 19