10. Usamakunkha khunkha la m'munda wako wamphesa, usamazitola zidagwazi za m'munda wako wamphesa; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
11. Musamaba, kapena kunyenga, kapena kunamizana.
12. Musamalumbira monama ndi kuchula dzina langa, ungaipse dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.
13. Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zace; mphotho yace ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m'mawa.
14. Usamatemberera wogontha; usamaika cokhumudwitsa pamaso pa wosaona; koma uziopa Mulungu wako; Ine ndine Yehova.
15. Musamacita cisalungamo pakuwemza mlandu; usamabvomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.
16. Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.
17. Usamamuda mbale wako mumtima mwako; umdzudzule munthu mnzako ndithu, usadzitengera ucimo cifukwa ca iye.
18. Usamabwezera cilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha; Ine ndine Yehova.
19. Muzisunga malemba anga, Usamalola zoweta zako za mitundu yosiyana zikwerane; usamabzala m'munda mwako mbeu za mitundu iwiri; usamabvala cobvala ca nsaru za mitundu iwiri zosokonezana.
20. Munthu akagona ndi mkazi, ndiye mdzakazi, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, wosamuombola kapena wosapatsidwa ufulu, akwapulidwe; asawaphe, popeza si mfulu mkaziyo.