Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 16:28-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndi iye amene anazitentha atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, ndipo atatero alowenso kucigono.

29. Ndipo lizikhala kwa Inu lemba Ilosatha; mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, muzidzicepetsa, osagwira Debito konse, kapena wa m'dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu;

30. popeza tsikuli adzacitira inu cotetezera, kukuyeretsani; adzakuyeretsani, kukucotserani zoipa zanu zonse pamaso pa Yehova.

31. Likhale kwa inu sabata lakupumula, kuti mudzicepetse; ndilo lemba losatha.

32. Ndipo wansembe, amene anamdzoza ndi kumdzaza dzanja lace acite nchito ya nsembe m'malo mwa atate wace, acite cotetezera, atabvala zobvala zabafuta, zobvala zopatulikazo.

33. Ndipo acite cotetezera malo opatulikatu, natetezere cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe; momwemo atetezerenso ansembe, ndi anthu onse a msonkhanowo.

34. Ndipo ici cikhale kwa inu lemba losatha, kucita cotetezera ana a Israyeli, cifukwa ca zocimwa zao zonse, kamodzi caka cimodzi. Ndipo anacita monga Yehova adauza Mose.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 16