Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 16:22-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. ndi mbuziyo isenze yokha mphulupulu zonsezo kumka nazo ku dziko la pa lokha; ndipo azitaya mbuziyo m'cipululu.

23. Pamenepo Aroni alowe m'cihema cokomanako, nabvule zobvala zabafuta zimene anazibvala polowa m'malo opatulika, nazisiye komweko.

24. Ndipo asambe thupi lace ndi madzi kumalo kopatulika, nabvale zobvala zace, naturuke, napereke nsembe yopsereza yace, ndi nsembe yopsereza ya anthu, nacite codzitetezera yekha ndi anthu.

25. Ndipo atenthe mafuta a nsembe yaucimo pa guwa la nsembe.

26. Ndipo iye amene anacotsa mbuzi ipite kwa Azazeli atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, ndipo atatero alowenso kucigono.

27. Koma ng'ombe ya nsembe yaucimo, ndi mbuzi ya nsembe yaucimo, zimene mwazi wao analowa nao kucita nao cotetezera m'malo opatulika, aturuke nazo kunja kwa cigono; natenthe ndi mota zikopa zao, ndi nyama zao, ndi cipwidza cao.

28. Ndi iye amene anazitentha atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, ndipo atatero alowenso kucigono.

29. Ndipo lizikhala kwa Inu lemba Ilosatha; mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi la mweziwo, muzidzicepetsa, osagwira Debito konse, kapena wa m'dziko, kapena mlendo wakukhala pakati panu;

30. popeza tsikuli adzacitira inu cotetezera, kukuyeretsani; adzakuyeretsani, kukucotserani zoipa zanu zonse pamaso pa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 16