Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 16:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, atamwalira ana amuna awiri a Aroni, muja anasendera pamaso pa Yehova, namwalira;

2. ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni mbale wako, kuti asalowe nthawi zonse m'malo opatulika m'tseri mwa nsaru yocinga, pali cotetezerapo cokhala palikasa, kuti angafe; popeza ndioneka mumtambo pacotetezerapo.

3. Aroni azilowa pa bwalo la malo opatulika nazozo: ng'ombe yamphongo ikhale ya nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale ya nsembe yopsereza.

4. Abvale maraya a m'kati a bafuta wopatulika, nakhale nazo zobvala za kumiyendo pathupi pace, nadzimangire m'cuuno ndi mpango wabafuta, nabvale nduwira yabafuta; izi ndi zobvala zopatulika; potero asambe thupi lace ndi madzi, ndi kubvala izi.

5. Ndipo ku khama la ana a Israyeli atenge atonde awiri akhale a nsembe yaucimo, ndi nkhosa yamphongo imodzi ikhale ya nsembe yopsereza.

6. Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yaucimo, ndiyo yace yace, nacite codzitetezera iye yekha, ndi mbumba yace.

7. Ndipo atenge mbuzi ziwirizo naziimike pamaso pa Yehova pakhomo pa cihema cokomanako.

8. Ndipo Aroniayesemaere pa mbuzi ziwirizo; maere amodzi kwa Yehova, ndi amodzi kwa Azazeli.

9. Ndipo Aroni abwere nayo mbuzi imene adaigwera maere a Yehova, naiyese nsembe yaucimo.

10. Koma mbuzi imene adaigwera maere a Azazeli, aiike yamoyo pamaso pa Yehova, kuti acite nayo cotetezera, kuitumiza kucipululu ikhale ya Azazeli.

11. Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yaucimo, ndiyo yace yace, nadzitetezere iye yekha, ndi mbumba yace, ndi kupha ng'ombe ya nsembe yaucimo ndiyo yace yace;

12. natenge mbale ya zofukiza yodzala ndi makara amoto, kuwacotsa pa guwa la nsembe, pamaso pa Yehova, ndi manja ace odzala ndi cofukiza copera ca pfungo lokoma, nalowe nayo m'tseri mwa nsaru yocinga;

13. naike cofukizaco pamoto pamaso pa Yehova, kuti mtambo wa cofukiza ciphimbe cotetezerapo cokhala pamboni, kuti angafe.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 16