Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 15:18-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.

19. Ndipo ngati mkazi ali ndi nthenda yakukha, ndi kukha kwace nkwa mwazi m'thupi mwace, akhale padera masiku asanu ndi awiri; ndipo ali yense amkhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

20. Ndipo cinthu ciri conse agonapo pokhala ali padera ncodetsedwa; ndi cinthu ciri conse akhalapo ncodetsa.

21. Ndipo ali yense akhudza kama wace azitsuka zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

22. Ndipo ali yense akhudza cinthu ciri conse akhalapo iye, atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

23. Ndipo cikakhala pakama, kapena pa cinthu ciri conse akhalapo iye, atacikhudza, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

24. Ndipo ngati mwamuna ali yense agona naye, ndi kudetsa kwace kukhala pa iye, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; ndipo kama ali yense agonapo ali wodetsedwa.

25. Ndipo mkazi akakhala ndi kukha mwazi masiku ambiri, osati masiku a kuoloka kwace, kapena akamakha kupitirira nthawi ya kuoloka kwace; masiku onse cirinkukha comdetsa cace, adzakhala wodetsedwa, monga masiku a kuoloka kwace.

26. Kama ali yense agonapo masiku a kukha kwace akhale ngati kama wa kuoloka kwace; ndi cinthu ciri conse akhalapo ciri codetsedwa, ngati kudetsa kwa kuoloka kwace.

27. Ndipo munthu ali yense akakhudza zimenezi adzakhala wodetsedwa, natsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

28. Koma akayeretsedwa kukha kwace, adziwerengere masiku asanu ndi awiri, ndipo atatero adzakhala woyeretsedwa.

29. Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike nazo kwa wansembe ku khomo la cihema cokomanako.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 15