Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 13:46-58 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

46. Masiku onse nthenda ikali pa iye azikhala wodetsedwa; ali wodetsedwa, agone pa yekha pokhala pace pakhale kunja kwa cigono.

47. Ndiponso ngati nthenda yakhate iri pa cobvala caubweya, kapena cathonje;

48. ngakhale iri pamuyaro, kapena pamtsendero, cathonje, kapena caubweya, ngakhale iri pa cikopa, kapena pa cinthu ciri conse copanga ndi cikopa;

49. ngati nthenda iri yobiriwira, kapena yofiira pacobvala, kapena pacikopa, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa, ndiyo nthenda yakhate; aziionetsa kwa wansembe;

50. ndipo wansembe aone nthendayo, nabindikiritse ciija ca nthenda masiku asanu ndi awiri;

51. naone nthenda tsiku lacisanu ndi ciwiri; ngati nthenda yakula pacobvala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pacikopa, ziri zonse zanchito zopangika ndi cikopa; nthendayo ndiyo khate lofukuta; ndico codetsedwa.

52. Ndipo atenthe cobvalaco ngakhale muyaro wace, ngakhale mtsendero wace, caubweya kapena cathonje, kapena ciri conse cacikopa ciri ndi khate, ndilo khate lofetsa; acitenrhe ndi mote.

53. Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda njosakula pacobvala, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa;

54. pamenepo wansembe aziuza kuti atsuke cija pali khate, nacibindikiritse masiku asanu ndi awiri ena;

55. ndipo wansembe aone nthenda ataitsuka, ndipo taonani, ngati nthendayi siinasandulika maonekedwe ace, yosakulanso nthenda, ndico codetsedwa; ucitenthe ndi moto; ndilo pfunka, kungakhale kuyera kwace kuli patsogolo kapena kumbuyo.

56. Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda yazimba ataitsuka, pamenepo aikadzule pa cobvala, kapena cikopa, kapena muyaro, kapena mtsendero;

57. ndipo ikaonekabe pacobvala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa cinthu ciri conse copangika ndi cikopa, irikubukanso; ucitenthe ndi moto cija canthenda.

58. Ndipo ukatsuka cobvalaco, kapena muyaro, kapena mtsendero, kapena cinthu ciri conse copangika ndi cikopa, ngati nthenda yalekapo pa cimeneco, acitsukenso kawiri, pamenepo ciri coyera.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 13