Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 13:29-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi nthenda pamutu kapena pandebvu,

30. wansembe aziona nthenda; ndipo taonani, ngati ioneka yokumba kubzola khungu, ndipo pali tsitsi loyezuka lotetemera; pamenepo wansembe amuche wodetsedwa; ndiyo mfundu, ndilo khate la mutu kapena ndebvu.

31. Ndipo wansembe akaona nthenda yamfundu, ndipo taonani, ioneka yosakumba kubzola khungu, ndipo palibe tsitsi lakuda pamenepo, wansembe ambindikiritse iye ali ndi mfundu masiku asanu ndi awiri;

32. ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri wansembe aone nthendayi; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula, ndipo mulibe tsitsi loyezuka, ndipo mfundu ikaoneka yosakumba kubzola khungu,

33. pamenepo azimeta, koma osameta pamfundu; ndipo wansembe ambindikiritse iye wamfundu masiku asanu ndi awiri ena;

34. ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri aone mfunduyo; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula pakhungu, ndipo ioneka yosakula kubzola khungu, wansembe amuche woyera, ndipo iye atsuke zobvala zace, nakhala woyera.

35. Koma ngati mfundu ikula pakhungu atachedwa woyera;

36. pamenepo wansembe amuone, ndipo taonani, ngati mfundu yakula pakhungu, wansembe asafunefune tsitsi loyezuka, ndiye wodetsedwa.

37. Koma monga momwe apenyera iye, ngati mfundu yaima pomwe, ndipo pamera tsitsi lakuda, mfundu yapola, ndiye woyera, ndipo wansembe amuche woyera.

38. Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi zikanga pa khungu la thupi lace, zikanga zoyerayera;

39. wansembe aziona; ndipo taonani ngati zikanga ziri pa khungu la thupi lao zikhala zotuwatuwa; ndilo thuza labuka pakhungu; ndiye woyera.

40. Ndipo ngati tsitsi la munthu lathothoka, ndiye wadazi; koma woyera.

41. Ndipo ngati tsitsi lathothoka pamphumi pace ndiye wa masweswe, koma woyera.

42. Koma ngati pali nthenda yotuuluka pakati pa dazi lace la pamutu, kapena la pamphumi, ndipo khate lirikubuka pakati pa dazi lace la pamutu, kapena la pamphumi.

43. Pamenepo wansembe azimuona, ndipo taonani, ngati cotupa cace ca nthenda ciri cotuuluka pa dazi la pa mutu wace, kapena la pamphumi pace, monga maonekedwe a khate pa khungu la thupi;

44. ndiye wakhate, ndiye wodetsedwa; wansembe amuchetu wodetsedwa; nthenda yace iri pamutu pace.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 13