Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 12:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2. Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Akaima mkazi, nakabala mwana wamwamuna, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; monga masiku ace akukhala padera, podwala iye, adzakhalawodetsedwa.

3. Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu adule khungu la mwanayo.

4. Ndipo akhale m'mwazi wa kumyeretsa kwace masiku makumi atatu kudza atatu; asakhudze kanthu kopatulika, kapena kulowa m'malo opatulika, kufikira adakwanira masiku a kumyeretsa kwace.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 12