Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 10:9-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Usamamwa vinyo, kapena coledzeretsa, iwe ndi ana ako omwe, m'mene mulowa m'cihema cokomanako, kuti mungafe; likhale lemba losatha mwa mibadwo yanu;

10. ndi kuti musiyanitse pakati pa copatulika ndi cosapatulika, ndi pakati pa codetsa ndi coyera;

11. ndi kuti muphunzitse ana a Israyeli malemba onse amene Yehova analankhula nao ndi dzanja la Mose.

12. Ndipo Mose ananena ndi Aroni, ndi Eleazara ndi Itamara, ana ace otsala, Tengani nsembe yaufa yotsalira ku nsembe zamoto za Yehova, ndi kuidya yopanda cotupitsa pafupi pa guwa la nsembe; pakuti ndiyo yopatulikitsa;

13. ndipo muziidyera kumalo kopatulika, popeza ndiyo gawo lako, ndi gawo la ana ako, locokera ku nsembe zamoto za Yehova; pakuti anandiuza cotero.

14. Ndi nganga yoweyula ndi mwendo wokweza mudyere izi pamalo poyera; iwe ndi ana ako amuna, ndi ana ako akazi omwe, popeza zapatsidwa gawo lako ndi gawo la ana ako amuna, zocokera ku nsembe zoyamika za ana a Israyeli.

15. Mwendo wokweza, ndi nganga yoweyula adze nazo pamodzi ndi nsembe zamoto zamafuta, aziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndipo zikhale zako ndi za ana ako amuna, mwa lemba losatha; monga Yehova anauza.

16. Ndipo Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yaucimo, ndipo, taonani, adaitentha.

17. Ndipo anapsa mtima pa Eleazara ndi Itamara, ana otsalawo a Aroni, nati, Mwalekeranji kudya nsembe yaucimo m'malo opatulika, pakuti ndiyo yopatulikitsa, ndipo iye anakupatsani iyo, kucotsera nayo mphulupulu ya khamulo, kuwacitira cowatetezera pamaso pa Yehova?

18. Taonani, sanalowa nao mwazi wace m'malo opatulika m'katimo; mukadaidyera ndithu m'malo opatulika, monga ndinakuuzani.

19. Ndipo Aroni analankhula ndi Mose, nati, Taonani, lero abwera nayo nsembe yao yaucimo ndi nsembe yao yopsereza pamaso pa Yehova; ndipo zandigwera zotere; ndikadadya nsembe yaucimo lero, kukadakomera kodi pamaso pa Yehova?

20. Pamene Mose adamva ici cidamkomera pamaso pace.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 10