Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 1:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. NDIPO Yehova anaitana Mose, nanena naye ali m'cihema cokomanako iye, nati,

2. Lankhula ndi ana a lsrayeli, nunene nao, Ali yense mwa inu akabwera naco copereka ca kwa Yehova, muzibwera naco copereka canu cikhale ca zoweta, ca ng'ombe, kapena ca nkhosa, kapena ca mbuzi.

3. Copereka cace cikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda cirema; abwere nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.

4. Ndipo aike dzanja lace pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwace, imtetezere.

5. Pamenepo aiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira pa guwa la nsembe, lokhala pa khoma la cihema cokomanako.

6. Ndipo asende nsembe yopsereza, ndi kuikadzula ziwalo zace.

7. Ndipo ana a Aroni asonkhe mota pa guwa la nsembe, ndi kukonza nkhuni pamotopo;

8. ndi ana a Aroni, ansembewo, akonze ziwalozo, mutu, ndi mafuta pa nkhuni ziri pa mota wa pa guwa la nsembe;

9. koma atsuke ndi madzi matumbo ace ndi miyendo yace; ndi wansembe atenthe zonsezi pa guwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.

10. Ndipo copereka cace cikakhala ca nkhosa, kapena ca mbuzi, cikhale nsembe yopsereza; azibwera nayo yaimuna yopanda cirema.

11. Ndipo aiphere iyo pa mbali ya kumpoto ya guwa la nsembe, pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 1