1. Usakondwera, Israyeli, ndi kusekerera, ngati mitundu ya anthu; pakuti wacita cigololo kuleka Mulungu wako, wakonda mphotho ya cigololo pa dwale la tirigu liri lonse.
2. Dwale ndi coponderamo mphesa sizidzawadyetsa, vinyo watsopano adzamsowa.
3. Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efraimu adza bwerera kumka ku Aigupto; ndipo adzadya cakudya codetsa m'Asuri.
4. Sadzatsanulira Yehova nsembe zavinyo; sizidzamkomera Iye nsembe zao; zidzakhala kwa iwo ngati mkate wa acisoni; onse akudyako adzadetsedwa; pakuti mkate wao udzakhala wa njala yao, uwu sudzalowa m'nyumbaya Yehova.
5. Mudzacitanji tsiku la masonkhano oikika, ndi tsiku la madyerero a Yehova?
6. Pakuti taonani, anacokera cionongeko, koma Aigupto adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m'manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m'mahema mwao.
7. Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israyeli adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, cifukwa ca kucuruka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukuru.
8. Efraimu ndiye wozonda kwa Mulungu wanga; kunena za mneneri, msampha wa msodzi uli m'njira zace zonse, ndi udani m'nyumba ya Mulungu wace.
9. Anadzibvunditsa kwambiri, monga masiku a Gibeya; adzakumbukila mphulupulu yao, adzalanga zocimwa zao.
10. Ndinapeza Israyeli ngati mphesa m'cipululu, ndinaona makolo anu ngati cipatso coyamba ca mkuyu nyengo yace yoyamba; koma anadza kwa Baala Peori, nadzipatulira conyansaco, nasandulika onyansa, conga cija anacikonda.
11. Kunena za Efraimu, ulemerero wao udzauluka ndi kucoka ngati mbalame; sipadzakhala kubala, ndi kukhala ndi pakati, ndi kuima.
12. Angakhale alera ana ao, koma ndidzawasowetsa, wosatsala munthu; ndithunso tsoka iwowa, pamene ndiwacokera.