Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 7:7-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Onsewo atentha ngati ng'anjo, natha oweruza ao, agwa mafumu ao onse; palibe mmodzi mwa iwo wakuitana Ine.

8. Efraimu asokonezana nayo mitundu ya anthu; Efraimu ndiye kamtanda ka mkate kosatembenuzidwa.

9. Alendo anatha mphamvu yace osacidziwaiye; imvi zomwe zampakiza osacidziwa iye,

10. Ndipo kudzikuza kwa Israyeli kumcitira umboni pamaso pace; koma sanabwerera kumka kwa Yehova Mulungu wao, kapena kumfunafuna mwa ici conse.

11. Ndipo Efraimu ali ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru; aitanira kwa Aigupto, amuka kwa Asuri.

12. Pamene amuka ndidzawayalira ukonde wanga, ndidzawagwetsa ngati mbalame za m'mlengalenga, ndidzawalanga monga udamva msonkhano wao.

13. Tsoka kwa iwowa! pakuti anandizembera; cionongeko kwa iwowa! pakuti anandilakwira; ndikadawalanditsa Ine, koma anandinenera zabodza.

14. Ndipo sanapfuulira kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.

15. Cinkana ndawalangiza ndi kulimbitsa manja ao, andilingiririra coipa,

16. Abwerera, koma si kwa Wam'mwambayo; akunga uta wosakhulupirika; akalonga ao adzagwa ndi lupanga mwa cipongwe ca lilime lao; ici ndico adzawasekera m'dziko la Aigupto.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 7