Abwerera, koma si kwa Wam'mwambayo; akunga uta wosakhulupirika; akalonga ao adzagwa ndi lupanga mwa cipongwe ca lilime lao; ici ndico adzawasekera m'dziko la Aigupto.