1. M'mene ndiciritsa Israyeli, mphulupulu ya Efraimu ibvumbuluka, ndi zoipa za Samariya; pakuti acita bodza, ndipo mkhungu alowa m'nyumba, ndi gulu la mbala manca kubwalo.
2. Ndipo sanena m'mtima mwao kuti Ine ndikumbukila zoipa zao zonse; tsopano macitidwe ao awazinga; ali pamaso panga,
3. Akondweretsa mfumu ndi zoipa zao, ndi akalonga ndi mabodza ao.
4. Acigololo onsewo; akunga ng'anjo anaitenthetsa wooca mkate; aleka kusonkha moto, poyambira kukanda mtanda kufikira watupa mtandawo.
5. Tsiku la mfumu yathu akalonga adzidwalitsa ndi kutentha kwa vinyo; iye anatambasula dzanja lace pamodzi ndi oseka.
6. Pakuti asendera nao mtima wao wakunga ng'anjo ya mkate, pokhala alikulalira; wooca mkate wao agona usiku wonse, m'mawa iyaka ngati moto wa malawi.
7. Onsewo atentha ngati ng'anjo, natha oweruza ao, agwa mafumu ao onse; palibe mmodzi mwa iwo wakuitana Ine.
8. Efraimu asokonezana nayo mitundu ya anthu; Efraimu ndiye kamtanda ka mkate kosatembenuzidwa.
9. Alendo anatha mphamvu yace osacidziwaiye; imvi zomwe zampakiza osacidziwa iye,
10. Ndipo kudzikuza kwa Israyeli kumcitira umboni pamaso pace; koma sanabwerera kumka kwa Yehova Mulungu wao, kapena kumfunafuna mwa ici conse.
11. Ndipo Efraimu ali ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru; aitanira kwa Aigupto, amuka kwa Asuri.
12. Pamene amuka ndidzawayalira ukonde wanga, ndidzawagwetsa ngati mbalame za m'mlengalenga, ndidzawalanga monga udamva msonkhano wao.
13. Tsoka kwa iwowa! pakuti anandizembera; cionongeko kwa iwowa! pakuti anandilakwira; ndikadawalanditsa Ine, koma anandinenera zabodza.
14. Ndipo sanapfuulira kwa Ine ndi mtima wao, koma alira pakama pao, asonkhanira tirigu ndi vinyo, apikisana ndi Ine.