Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Hoseya 2:15-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo ndidzampatsa minda yace yamphesa kuyambira pomwepo, ndi cigwa ca Akori cikhale khomo la ciyembekezo; ndipo adzabvomereza pomwepo monga masiku a ubwana wace, ndi monga tsiku lokwera iye kuturuka m'dziko la Aigupto.

16. Ndipo kudzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova, udzandicha Mwamuna wanga, osandichanso Baala wanga.

17. Pakuti ndidzacotsa maina a Abaala m'kamwa mwace; ndipo silidzakumbukikanso dzina lao.

18. Ndipo tsiku lomwelo ndidzawacitira pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; ndipo ndidzatyola uta, ndi lupanga, ndi nkhondo, zicoke m'dziko, ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.

19. Ndipo ndidzakutomera ukhale wanga kosatha, inde ndidzakutomera ukhale wanga m'cilungamo, ndi m'ciweruzo, ndi m'ukoma mtima, ndi m'cifundo.

20. Ndidzakutomeranso ukhale wanga mokhulupirika, ndipo udzadziwa Yehova.

21. Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, ndidzabvomereza, ati Yehova, ndidzabvomereza thambo, ndi ilo lidzabvomereza dziko lapansi;

22. ndi dziko lapansi lidzabvomereza tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta; ndi izi zidzabvomereza Yezreeli.

23. Ndipo ndidzadzibzalira iye m'nthaka, ndipo ndidzacitira cifundo Wosacitidwa-cifundo; ndipo ndidzati kwa Si-anthu-anga, Muli anthu anga; ndipo iwo adzati, Ndinu Mulungu wathu.

Werengani mutu wathunthu Hoseya 2