Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Habakuku 3:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Mapiri anakuonani, namva zawawa;Cigumula ca madzi cinapita;Madzi akuya anamveketsa mau ace,Nakweza manja ace m'mwamba.

11. Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao;Pa kuunika kwa mibvi yanu popita iyo.Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.

12. Munaponda dziko ndi kulunda,Munapuntha amitundu ndi mkwiyo.

13. Munaturukira cipulumutso ca anthu anu,Cipulumutso ca odzozedwa anu;Munakantha mutu wa nyumba yawoipa,Ndi kufukula maziko kufikira m'khosi.

14. Munapyoza ndi maluti ace mutu wa ankhondo ace;Anadza ngati kabvumvulu kundimwaza;Kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mabisika.

15. Munaponda panyanja ndi akavaloanu,Madzi amphamvu anaunjikana mulu.

16. Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka,Milomo yanga inanthunthumira pamau,M'mafupa mwanga mudalowa cibvundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga;Kuti ndipumule tsiku lamsauko,Pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.

17. Cinkana mkuyu suphuka,Kungakhale kulibe zipatso kumpesa;Yalephera nchito ya azitona,Ndi m'minda m'mosapatsa cakudya;Ndi zoweta zacotsedwa kukhola,Palibenso ng'ombe m'makola mwao;

18. Koma ndidzakondwera mwa Yehova,Ndidzasekerera mwa Mulungu wa cipulumutso canga.

Werengani mutu wathunthu Habakuku 3