Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 9:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo Ine, taonani, Ine ndikhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu, ndi mbeu zanu pambuyo panu;

10. ndi zamoyo zonse ziti pamodzi ndi inu, zouluka, ng'ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zoturuka m'cingalawa, zinyama zonse za dziko lapansi,

11. Ndipo ndidzakhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu; zamoyo zonse sizidzamarizidwanso konse ndi madzi a cigumula; ndipo sikudzakhalanso konse cigumula cakuononga dziko lapansi.

12. Ndipo anati Mulungu, Ici ndici cizindikiro ca pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse ziti pamodzi ndi inu, ku mibadwo mibadwo;

13. ndiika Uta-wa-Leza wanga m'mtambomo, ndipo udzakhala cizindikiro ca pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi.

14. Ndipo padzakhala popimba ndi mtambo Ine dziko lapansi, utawo udzaoneka m'mtambomo;

15. ndipo ndidzakumbukira pangano langa limene liri ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo; ndipo madzi sadzakhalanso konse cigumula cakuononga zamoyo zonse.

16. Ndipo utawo udzakhala m'mtambo; ndipo ndidzauyang'anira kuti ndikumbukire pangano lacikhalire liri ndi Mulungu ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo pa dziko lapansi.

17. Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ici ndici cizindikiro ca pangano ndalikhazikitsa popaogana ndi Ine ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 9