Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 50:15-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo pamene abale ace a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamcitira iye.

16. Ndipo anatumiza mthenga kwa Yosefe kuti, Atate wathu asanafe analamulira, kuti,

17. Muziti cotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kucimwa kwao, cifukwa kuti anakucitirani inu coipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa aka polo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye.

18. Ndiponso abale ace anamuka namgwadira pamaso pace; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu.

19. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Musaope; pakuti ndiri ine kodi m'malo a Mulungu?

20. Koma inu, munandipangira ine coipa; koma Mulungu anacipangira cabwino, kuti kucitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri,

21. Ndipo tsopano musaope; Ine ndidzacereza inu, ndi ana anu ang'ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yao, nanena nao mokoma mtima.

22. Ndipo Yosefe anakhala m'Aigupto, iye, ndi mbumba ya atate wace; ndipo Yosefe anakhala ndi movo zaka zana limodzi ndi khumi.

23. Ndipo Yosefe anaona ana a Efraimu a mbadwo wacitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.

24. Yosefe ndipo anati kwa abale ace, Ndirinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakucotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isake, ndi kwa Yakobo

Werengani mutu wathunthu Genesis 50