Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 50:11-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo; Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro akuru a Aaigupto: cifukwa cace dzina la pamenepo linachedwa Abeli-mizraimu, pali tsidya lija la Yordano.

12. Ndipo ana ace amuna anamcitira iye monga anawalamulira iwo;

13. cifukwa kuti ana ace amuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pace, kwa Efroni Mhiti, patsogolo pa Mamre.

14. Ndipo ataika atate wace, Yosefe mabwera ku Aigupto, iye ndi abale ace, ndi onse amene anakwera pamodzi naye kukaika atate wace.

15. Ndipo pamene abale ace a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamcitira iye.

16. Ndipo anatumiza mthenga kwa Yosefe kuti, Atate wathu asanafe analamulira, kuti,

17. Muziti cotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kucimwa kwao, cifukwa kuti anakucitirani inu coipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa aka polo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye.

18. Ndiponso abale ace anamuka namgwadira pamaso pace; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu.

19. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Musaope; pakuti ndiri ine kodi m'malo a Mulungu?

20. Koma inu, munandipangira ine coipa; koma Mulungu anacipangira cabwino, kuti kucitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri,

21. Ndipo tsopano musaope; Ine ndidzacereza inu, ndi ana anu ang'ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yao, nanena nao mokoma mtima.

22. Ndipo Yosefe anakhala m'Aigupto, iye, ndi mbumba ya atate wace; ndipo Yosefe anakhala ndi movo zaka zana limodzi ndi khumi.

23. Ndipo Yosefe anaona ana a Efraimu a mbadwo wacitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.

24. Yosefe ndipo anati kwa abale ace, Ndirinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakucotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isake, ndi kwa Yakobo

25. Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israyeli kuti, Mulungu adzaonekera kwa inu ndithu, ndipo mudzakwera nao mafupa anga kucokera kuno.

26. Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lace ndi mankhwala osungira, ndipo ariamuika iye m'bokosi m'Aigupto.

Werengani mutu wathunthu Genesis 50