Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 47:24-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndipo padzakhala pakukunkha, muzipatsa limodzi la mwa magawo asanu kwa Farao, koma magawo anai ndi anu, mbeu za munda, ndi za cakudya canu, ndi ca ana anu ndi mabanja anu.

25. Ndipo iwo anati, Watipulumutsa miyoyo yathu; tipeze ufulu pamaso pa mbuyanga, ndipo tidzakhala akapolo a Farao.

26. Ndipo Yosefe analamulira lamulo la pa dziko la Aigupto kuukira lero, kuti Farao alandire limodzi la mwa magawo asanu; koma dziko la ansembe lokha silinakhala la Farao.

27. Ndipo Israyeli anakhala m'dziko la Aigupto, m'dziko la Goseni; nakhala nazo zaozao m'menemo, nabalana nacuruka kwambiri.

28. Ndipo Yakobo anakhala m'dziko la Aigupto zaka khumi mphambu zisanu ndi ziwiri; ndipo masiku a Yakobo zaka za moyo wace zinali zaka zana limodzi mphambu makumi anai kudza zisanu ndi ziwiri.

29. Ndipo nthawi inayandikira kuti Israyeli adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wace wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ncafu yanga, nundicitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine m'Aigupto;

30. koma pamene ndidzagona ndi makolo anga, udzanditenge ine kuturuka m'dziko la Aigupto, ukandiike ine m'manda mwao. Ndipo iye anati, Ndidzacita monga mwanena.

31. Ndipo anati, Undilumbirire ine; namlumbirira iye. Ndipo Israyeli anawerama kumutu kwa kama.

Werengani mutu wathunthu Genesis 47