Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 45:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yosefe sanakhoza kudziletsa pamaso pa onse amene anaima naye: nati, Turutsa anthu onse pamaso panga. Ndipo panalibe munthu pamodzi ndi iye pamene Yosefe anadziululira yekha kwa abale ace.

2. Ndipo analira momveka, ndipo anamva Aaigupto, ndipo anamva a m'nyumba ya Farao.

3. Ndipo Yosefe anati kwa abale ace, Ine ndine Yosefe; kodi-akali ndi moyo atate wanga? Ndipo abale ace sanakhoza kumyankha iye; pakuti anabvutidwa pakumuona iye.

4. Ndipo Yosefe anati kwa abale ace, Muyandikiretu kwa ine; nayandikira. Ndipo iye anati, Ine ndine Yosefe mbale wanu, ine ndemwe munandigulitsa ndilowe m'Aigupto.

5. Tsopano musaphwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha, kuti munandigulitsira ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo.

6. Zaka ziwirizi muli njala m'dziko muno; ndipo zatsala zaka zisanu, zopanda kulima kapena kusenga,

7. Ndipo Mulungu anatumiza ine patsogolo panu kuti ndikhazike inu mutsale m'dziko lapansi, ndi kusunga inu amoyo ndi cipulumutso cacikuru.

8. Ndipo tsopano sindinu amene munanditumiza ine ndifike kuno, koma Mulungu, ndipo anandiyesa ine atate wa Farao, ndi mwini banja lace lonse, ndi wolamulira dziko lonse la Aigupto.

Werengani mutu wathunthu Genesis 45