Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 43:8-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo Yuda anati kwa atate wace Israyeli, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono.

9. Ine ndidzakhala cikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, cifukwa cace cidzakhala pa ine masiku onse:

10. pakuti tikadaleka kucedwa mwenzi tsopano titabwera kawiri.

11. Ndipo Israyeli atate wao anati kwa iwo, Ngati comweco tsopano citani ici: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta a mankhwala pang'ono, ndi uci pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;

12. nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanacita dala;

13. mutengenso mphwanu, nimuoyamuke, mupitenso kwa munthu uja:

14. Mulungu Wamphamvuyonse adzakupatsani inu cifundo pamaso pa munthu uja, kuti akumasulireni inu mbale wanu wina ndi Benjamini. Ndipo ine, ngati ndikhala wopanda ana, ndikhalatu.

15. Amunawo ndipo anatenga mphatso, natenga ndalama zowirikiza m'manja mwao, ndi Benjamini; ndipo ananyamuka ndi kutsikira ku Aigupto, naima pamaso pa Yosefe.

16. Ndipo pamene anaona Benjamini pamodzi nao, anati kwa tsanyumba wace, Lowa nao anthuwo m'nyumba, kaphere iwo, kakoozere, cifukwa anthuwo adzadya ndi ine usana uno.

Werengani mutu wathunthu Genesis 43