Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 43:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo njala inakula m'dzikomo.

2. Ndipo panali pamene atatha kudya tirigu yense anatengayo ku Aigupto atate wao anati kwa iwo, Pitaninso, mukatigulire ife cakudya pang'ono.

3. Ndipo Yuda ananena ndi iye kuti, Munthu uja anatilimbitsira mau kuti, Simudzaonanso nkhope yanga, koma mphwanu akhale ndi inu ndiko.

4. Ngati mudzatuma mphwathu pamodzi ndi ife, tidzatsikira ndi kugulira inu cakudya.

5. Koma mukapanda kumtuma iye sititsika; pakuti munthu uja anati kwa ife, Simudzaona nkhope yanga, ngati mphwanu sali ndi inu.

6. Ndipo Israyeli anati, Cifukwa ninji munandicitira ine coipa cotero kuti munamuuza munthuyo muli ndi mphwanu?

7. Ndipo iwo anati, Munthuyo anafunsitsa za ife, ndi za abale athu, kuti, Atate wanu alipo? Kodi muli ndi mphwanu? ndipo tinamfotokozera iye monga mwa mau amenewo: ngati tinadziwa kuti iye adzati, Idzani naye mphwanu?

8. Ndipo Yuda anati kwa atate wace Israyeli, Mumtume mnyamata pamodzi ndi ine ndipo ife tidzanyamuka ndi kupita; kuti tikhale ndi moyo tisafe, ife ndi inu ndi ana athu ang'ono.

9. Ine ndidzakhala cikole, pa manja anga mudzamfunsa: ndikapanda kumbwezera kwa inu ndi kumuimitsa pamaso panu, cifukwa cace cidzakhala pa ine masiku onse:

10. pakuti tikadaleka kucedwa mwenzi tsopano titabwera kawiri.

11. Ndipo Israyeli atate wao anati kwa iwo, Ngati comweco tsopano citani ici: tengani zipatso za m'dziko muno m'zotengera zanu, mumtengere munthu uja mphatso, mafuta a mankhwala pang'ono, ndi uci pang'ono, zonunkhira ndi mure, ndi mfula, ndi katungurume;

12. nimutenge ndalama zowirikiza m'manja mwanu; ndipo ndalama zimene zinabwezedwa kukamwa kwa matumba anu mutengenso m'manja mwanu; kapena sanacita dala;

Werengani mutu wathunthu Genesis 43