Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 42:31-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Koma ife tinati kwa iye, Tiru anthu oona; sitiri ozonda;

32. tiri abale khumi ndi awiri, ana a atate wathu; wina palibe, ndipo lero wamng'ono ali ndi atate wathu m'dziko la Kanani.

33. Ndipo munthuyo mwini dziko anati kwa ife, Momwemu ndidzadziwa kuti muli anthu oona; siyani mmodzi wa abale anu pamodzi ndi ine, tengani tirigu wa njala ya kwanu, mukani;

34. idzani naye mphwanu kwa ine, ndipo ndidzadziwa kuti simuli ozonda koma anthu oona: comweco ndidzakubwezerani inu mbale wanu, ndipo mudzacita malonda m'dziko muno.

35. Ndipo panali pamene analikukhuthula matumba ao, taonani, phukusi la ndalama la yense linali m'thumba lace; ndipo pamene iwo ndi atate ao anaona mapukusi a ndalama anaopa,

36. Ndipo Yakobo atate wao anati kwa iwo, Munandilanda ine ana; Yosefe palibe, Simeoni palibe, ndipo mudzacotsa Benjamini: zonse zimene zandigwera.

37. Ndipo Rubeni anati kwa atate wace, kuti, Muwaphe ana anga amuna awiri ndikapanda kumbweza iye kwa inu; mumpereke iye m'manja mwanga, ndipo ine ndidzambwezanso kwa inu.

38. Ndipo iye anati, Mwana wanga sadzatsikira ndi inu, cifukwa kuti mkuru wace wafa, ndipo watsala iye yekha; ngati coipa cikamgwera iye m'njira m'mene mupitamo, inu mudzatsitsira ndi cisoni imvi zanga kumanda.

Werengani mutu wathunthu Genesis 42