Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 41:41-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Taona, ndakhazika iwe wolamulira dziko lonse la Aigupto.

42. Ndipo Farao anacotsa mphete yosindikizira yace pa dzanja lace, naibveka pa dzanja la Yosefe, nambveka iye ndi zobvalira zabafuta, naika unyolo wagolidi pakhosi pace;

43. ndipo anamkweza iye m'gareta wace waciwiri amene anali naye: ndipo anapfuula patsogolo pa iye, Gwadani; ndipo anamkhazika iye wolamulira dziko lonse la Aigupto,

44. Ndipo Farao anati kwa Yosefe, Ine ndine Farao, ndipo popanda iwe palibe munthu ali yense adzatukula dzanja lace kapena mwendo wace m'dziko lonse la Aigupto.

45. Ndipo Farao anamucha dzina la Yosefe Zafenati-Panea; ndipo anampatsa akwatire Asenati mwana wamkazi wa Potifera wansembe wa Oni. Ndipo Yosefe anaturuka wolamulira, nayendayenda m'dziko la Aigupto.

46. Ndipo Yosefe anali wa zaka makumi atatu pamene iye anaima pamaso pa Farao mfumu ya Aigupto, Ndipo Yosefe anaturuka pamaso pa Farao, napitapita pa dziko lonse la Aigupto,

47. Ndipo zaka zisanu ndi ziwiri zakucuruka dzinthu nthaka inabala zambirimbiri.

Werengani mutu wathunthu Genesis 41