Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 41:15-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Farao ndipo anati kwa Yosefe, Ine ndalota loto, koma palibe wondimasulira; ndipo ndamva alikunena za iwe kuti, ukamva loto udziwa kumasulira.

16. Ndipo Yosefe anayankha Farao kuti, Si mwa ine; koma Mulungu adzayankha Farao mwamtendere.

17. Ndipo Farao ananena kwa Yosefe, M'loto langa taona, ndinaima m'mphepete mwa nyanja;

18. ndipo taona, zinaturuka m'nyanjamo ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri, zonenepa ndi za maonekedwe abwino; ndipo zinadya m'mabango;

19. ndipo, taona, ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zina zinaturuka pambuyo pao zosauka ndi za maonekedwe oipa ndi zoonda, zoipa zotere sindinazione m'dziko la Aigupto;

20. ndipo ng'ombe zazikazi zoonda ndi za maonekedwe oipa zinadya ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zonenepa,

21. Ndipo pamene zinadya sizinadziwika kuti zinadya; koma zinaipabe m'maonekedwe ao monga poyamba.

22. Pamenepo ndinauka. Ndipo ndinaona m'kulota kwanga, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zinamera pa mbuwa imodzi zodzala ndi zabwino;

23. ndipo, taona, ngala zisanu ndi ziwiri zina zofota, zoonda, zopsyerera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao;

24. ndipo ngala zoonda zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zabwino; ndipo ndinafotokozera amatsenga: koma panalibe wondimasulira ine.

25. Ndipo Yosefe anati kwa Farao, Loto la Farao liri limodzi: cimene Mulungu ati acite wammasulira Farao.

26. Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndi ngala zisanu ndi ziwiri zabwino ndizo zaka zisanu ndi ziwiri: loto liri limodzi.

27. Ng'ombe zazikazi zisanu ndi ziwiri zoonda ndi za maonekedwe oipa zinaturuka pambuyo pao ndizo zaka zisanu ndi ziwiri, ndiponso ngala zisanu ndi ziwiri zopanda kanthu zopsyerera ndi mphepo ya kum'mawa, ndizo zaka zisanu ndi ziwiri za njala.

28. Ici ndi cinthu cimene ndinena kwa Farao: cimene Mulungu ati acite wasonyeza kwa Farao.

Werengani mutu wathunthu Genesis 41