Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 39:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo Yehova anali ndi Yosefe; ndipo iye anali wolemeralemera; nakhala m'nyumba ya mbuyace M-aigupto.

3. Ndipo mbuyace anaona kuti Yehova anali ndi iye, ndi kuti Yehova anamlemereza m'dzanja lace zonse anazicita.

4. Ndipo Yosefe anapeza ufulu pamaso pace, ndipo anamtumikira iye; ndipo anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yace, naika m'manja mwace zonse anali nazo.

5. Ndipo panali ciyambire anamuyesa iye woyang'anira pa nyumba yace, ndi pa zace zonse, Yehova anadalitsa nyumba ya M-aigupto cifukwa ca Yosefe; ndipo mdalitso wa Yehova unali pa zace zonse, m'nyumba ndi m'munda.

6. Ndipo iye anasiya zace zonse m'manja a Yosefe; osadziwa comwe anali naco, koma cakudya cimene anadya. Ndipo Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola.

7. Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyace anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine.

8. Koma iye anakana, nati kwa mkazi wa mbuyace, Taonani, mbuyanga sadziwa cimene ciri ndi ine m'nyumbamu, ndipo anaika zace zonse m'manja anga;

Werengani mutu wathunthu Genesis 39