Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 38:15-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Pamene Yuda anamuona iye, anaganizira kuti ali mkazi wadama: cifukwa iye anabisa nkhope yace.

16. Ndipo iye anapatukira kwa mkazi panjira, nati, Tiyetu, ndilowane nawe; cifukwa sanamdziwa kuti ndiye mpongozi wace. Ndipo anati, Kodi udzandipatsa ine ciani kuti ulowane ndi ine.

17. Ndipo iye anati, Ndidzatumiza kwa iwe kamwana ka mbuzi ka m'ziweto. Ndipo mkazi nati, Kodi udzandipatsa ine cikole mpaka ukatumiza?

18. Ndipo iye anati, Cikole canji ndidzakupatsa iwe? Ndipo mkazi anati, Mphete yako, ndi cingwe cako, ndi ndodo iri m'dzanja lako. Ndipo anampatsa izo, nalowana naye, ndipo mkazi anatenga pakati ndi iye.

19. Ndipo mkazi anauka nacoka, nabvula copfunda cace, nabvala zobvala zamasiye zace.

20. Ndipo Yuda anatumiza kamwana ka mbuzi ndi dzanja la bwenzi lace Madulami, kuti alandire cikole pa dzanja la mkazi; koma sanampeza iye.

21. Ndipo anafunsa amuna a pamenepo kuti, Ali kuti wadama uja anali pambali pa njira pa Enaimu? ndipo iwo anati, Panalibe wadama pano.

Werengani mutu wathunthu Genesis 38