Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 35:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Beteli nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako.

2. Ndipo Yakobo anati kwa a banja lace, ndi kwa onse amene anali ndi iye, Cotsani milungu yacilendo iri mwa inu, mudziyeretse, ndi kupindula zobvala zanu:

3. tinyamuke, tikwere tinke ku Beteli: ndipo tidzamanga kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anandibvomereza tsiku la mabvuto anga, ndiponso anali ndi ine m'njira m'mene ndinapitamo.

4. Ndipo anampatsa Yakobo milungu yacilendo yonse inali m'manja mwao, ndi mphete zinali m'makutu mwao: ndipo Yakobo anazibisa pansi pa mtengo wathundu unali pa Sekemu.

5. Ndipo anapita, ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera midzi yakuwazinga, ndipo sanalondola ana a Yakobo.

6. Ndipo Yakobo anafika ku Luzi, ndiko ku dziko la Kanani (ndiwo Beteli), iye ndi anthu onse anali pamodzi ndi iye.

7. Ndipo anamanga kumeneko guwa la nsembe, Dacha pamenepo El Beteli: pakuti kumeneko Mulungu anaonekera kwa iye muja anathawa pa nkhope ya mbale wace.

8. Ndipo anafa Debora mlezi wa Rebeka, naikidwa kunsi kwa Beteli, pansi pa mtengo wathundu; ndipo anacha dzina lace AlioniBakuti.

9. Ndipo Mulungu anamuonekeranso Yakobo, pamene iye anacokera m'Padanaramu, namdalitsa iye.

Werengani mutu wathunthu Genesis 35