Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 31:31-45 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Ndipo anayankha Yakobo nati kwa Labani, Cifukwa ndinaopa: cifukwa kuti, ndinati, Kapena udzandilanda ine ana ako akazi.

32. Ali yense umpeza ali nayo milungu yako, asakhale ndi movo: pamaso pa abale athu, tayang'anira zako ziri ndi ine, nuzitenge wekha. Pakuti sanadziwe Yakobo kuti Rakele anaiba.

33. Ndipo Labani analowa m'hema wa Yakobo, ndi m'hema wa Leya, ndi m'mahema a adzakazi awiri aja; koma sanapeze, Ndipo anaturuka m'hema wa Leya nalowa m'hema wa Rakele.

34. Ndipo Rakele anatenga aterafiwo nabisa pa cokhalira ca ngamila, nakhala pamenepo, Ndipo Labani anafunafuna m'hema monse, koma sanawapeze.

35. Ndipo Rakele anati kwa atate wace, Asakwiye mbuyanga kuti sindingathe kuuka pamaso panu; cifukwa zocitika pa akazi ziri pa ine. Ndipo Labani anafunafuna koma sanapeze aterafiwo.

36. Ndipo anakwiya Yakobo namkalipira Labani: ndipo Yakobo anayankha nati kwa Labani, Kodi ndacimwa ciani? ucimo wanga nguti, kuti unanditsatatsata ine pambuyo panga?

37. Pakuti wafunafuna monse ndiri nazo, kodi wapeza ciani pa zinthu za m'nyumba mwako? Tafika naco apa pa abale anga ndi ako, kuti aweruze pa ife tonse awiri.

38. Zaka makumi awiriwo ndakhala nawe, nkhosa ndi mbuzi zako zazikazi sizinapoloze, ndi abira a zoweta zako sindinadye.

39. Cimene cinazomoledwa ndi cirombo sindinacitengere kwa iwe; ndekha ndinalipira; pa dzanja langa unacifuna, cingakhale cobedwa kapena pausiku kapena pausana.

40. Cotero ndinakhala; usana ludzu linakomola ine, usiku cisanu; tulo tanga tinacoka m'maso mwanga.

41. Ndinakhala cotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe cifukwa ca ana ako akazi awiri, ndi zaka zisanu ndi cimodzi cifukwa ca zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.

42. Mulungu wa atate wanga, Mulungu wa Abrahamu, ndi Kuopsa kwa Isake zikadapanda kukhala ndi ine, ukadandicotsa ine wopanda kanthu m'manja. Mulungu anakuona kusauka kwanga, ndi nchito ya manja anga, ndipo anadzudzula iwe usiku walero.

43. Ndipo Labani anayankha nati kwa Yakobo, Akaziwa ndiwo ana anga, anawa ndiwo ana anga, zowetazi ndizo zoweta zanga ndi zonse ulinkuziona ndizo zanga: nanga ndidzacitira ine ciani lero kwa ana anga akazi amenewa, kapena ana ao amene anabala?

44. Tsopano tiyeni tipangane pangano, ine ndi iwe; likhale mboni pakati pa ine ndi iwe.

45. Ndipo Yakobo anatenga mwala, nauimiritsa.

Werengani mutu wathunthu Genesis 31