Ndipo Rakele anati kwa atate wace, Asakwiye mbuyanga kuti sindingathe kuuka pamaso panu; cifukwa zocitika pa akazi ziri pa ine. Ndipo Labani anafunafuna koma sanapeze aterafiwo.