Ndipo Labani anayankha nati kwa Yakobo, Akaziwa ndiwo ana anga, anawa ndiwo ana anga, zowetazi ndizo zoweta zanga ndi zonse ulinkuziona ndizo zanga: nanga ndidzacitira ine ciani lero kwa ana anga akazi amenewa, kapena ana ao amene anabala?