Ndinakhala cotere zaka makumi awiri m'nyumba mwako; zaka khumi ndi zinai ndinakutumikira iwe cifukwa ca ana ako akazi awiri, ndi zaka zisanu ndi cimodzi cifukwa ca zoweta zako; wasintha malipiro anga kakhumi.