Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 28:13-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Taonani, Yehova anaima pamwamba pace, nati, Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abrahamu atate wako, ndi Mulungu wa Isake; dziko limene ulinkugonamo ndidzakupatsa Iwe ndi mbeu zako;

14. mbeu zako zidzakhala monga pfumbi lapansi, ndipo udzabalalikira kumadzulo ndi kum'mawa ndi kumpoto ndi kumwera: mwa iwe ndi mu mbeu zako mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa.

15. Taonani, Ine ndiri pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; cifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditacita cimene ndanena nawe.

16. Ndipo Yakobo anauka m'tulo tace, nati, Ndithu, Yehova ali mommuno; ndipo sindinadziwe.

17. Ndipo anaopa, nati, Poopsya pompano! pompano ndipo pa nyumba ya Mulunga, si penai, pompano ndipo pa cipata ca kumwamba.

18. Yakobo ndipo anauka m'mamawa, natenga mwala umene anaika pansi pa mutu wace, nauimiritsa, nathira mafuta pamtu pace.

19. Ndipo anacha dzina la pamenepo Beteli; pakuyamba dzina lace la mudziwo ndi Luzi.

20. Yakobo ndipo analumbiracilumbiro, nati, Mulungu akakhala ndi ine, akandisunga ine m'njira imene ndipitamo, akandipatsa ine mkate wa kudya, ndi zobvalira za kubvala,

21. kuti ndibwerenso ku nyumba ya atate wanga ndi mtendere, pamenepo Yehova adzakhala Mulungu wanga,

22. ndi mwala umenewu ndinauimiritsa, udzakhala nyumba ya Mulungu; ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani Inu limodzi la magawo khumi.

Werengani mutu wathunthu Genesis 28