Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 26:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali njala padzikopo, yoyenjezeka ndi njala yoyamba ija imene inali masiku a Abrahamu, ndipo Isake ananka kwa Abimeleke mfumu ya Afilisti ku Gerari.

2. Ndipo Yehova anamuonekera iye nati, Usatsikire ku Aigupto, khala m'dziko m'mene ndidzakuuza iwe;

3. khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe cifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa cilumbiriro ndinacilumbirira kwa Abrahamu atate wako;

4. ndipo ndidzacurukitsa mbeu zako monga nyenyezi za kumwamba, ndipo ndidzapatsa mbeu zako maiko onsewa; m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa;

5. cifukwa kuti Abrahamu anamvera mau anga, nasunga cilangizo canga, ndi maweruziro anga, ndi malemba anga ndi malamulo anga.

6. Ndipo Isake anakhala m'Gerari;

7. ndipo anthu a kumeneko anamfunsa iye za mkazi wace; ndipo iye anati, diye mlongowanga: cifukwa kuti anaopa kunena, Mkazi wanga; anati, anthu a kumeneko angandiphe ine cifukwa ca Rebeka; popeza anali wokongola pakumuona.

8. Ndipo panali atakhala komwe masiku ambiri, Abimeleke mfumu ya Afilisti, anayang'ana kunja kwa zenera, napenya, taona, Isake analinkuseka ndi Rebeka mkazi wace.

9. Ndipo Abimeleke anamuitana Isake nati, Taona, uyo ndi mkazi wako ndithu: kodi bwanji unati, Ndiye mlongo wanga? Ndipo Isake anati kwa iye, Cifukwa ndinati, Ndingafe cifukwa ca iye.

10. Ndipo Abimeleke anati, Nciani cimeneci waticitira ife? panatsala pang'ono ena a anthu akadagona naye mkazi wako, ndipo ukadaticimwitsa ife:

Werengani mutu wathunthu Genesis 26