Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 23:13-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo ananena kwa Efroni alinkumva anthu a m'dzikomo, kuti, Koma ngati ufuna, undimveretu ine: ndidzakupatsa iwe mtengo wace wa munda; uulandire kwa ine, ndipo ndidzaika wakufa wanga m'menemo.

14. Ndipo Efroni anamyankha Abrahamu, nati kwa iye,

15. Mfumu, mundimvere ine; kadziko ka mtengo wace wa masekele a siliva mazana anai, ndiko ciani pakati pa ine ndi inu? ikani wakufa wanu.

16. Ndipo Abrahamu anamvera Effoni, ndipo Abrahamu anamuyesera Efroni ndalama zimene ananena alinkumva ana a Heti, masekele a siliva mazana anai, ndalama zomwezo agulana nazo malonda.

17. Ndipo munda wa Efroni umene unali m'Makipela, umene unali patsogolo pa Mamre, munda ndi phanga liri momwemo, ndi mitengo yonse inali m'mundamo, yokhala m'malire monse mozungulira momwemo,

18. inalimbitsidwa kwa Abrahamu ikhale yace, pamaso pa ana a Heti, pa onse amene analowa pa cipata ca mudzi wace.

19. Zitatha izi Abrahamu anaika Sara mkazi wace m'phanga la munda wa Makipela patsogolo pa Mamre (ndiwo Hebroni), m'dziko la Kanani.

20. Ndipo ana a Heti analimbitsira Abrahamu munda, ndi phanga liri m'menemo, likhale lace lamanda.

Werengani mutu wathunthu Genesis 23