Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Genesis 21:7-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo anati, Akadatero ndani kwa Abrahamu kuti Sara adzayamwitsa ana? pakuti ndambalira iye mwana wamwamuna m'ukalamba wace.

8. Ndipo anakula mwanayo naletsedwa kuyamwa: ndipo Abrahamu anakonza madyerero akuru tsiku lomwe analetsedwa Isake kuyamwa.

9. Ndipo Sara anaona mwana wace wamwamuna wa Hagara M-aigupto, amene anambalira Abrahamu, alinkuseka.

10. Cifukwa cace anati kwa Abrahamu, Cotsa mdzakazi uyo, ndi mwana wace wamwamuna; cifukwa mwana wa mdzakazi uyo sadzalowa m'nyumba pamodzi naye mwana wanga Isake.

11. Ndipo mauwo anaipira Abrahamu cifukwa ca mwana wace.

12. Ndipo Mulungu anati kwa Abrahamu, Usaipidwe nao, cifukwa ca mnyamatayo, ndi cifukwa ca mdzakazi wako; momwe monse akunenera iwe Sara umvere iwe mau ace; cifukwa kuti mwa Isake zidzaitanidwa mbeu zako.

13. Ndipo mwana wamwamuna wa mdzakazi uyo ndidzayesa mtundu, cifukwa iye ndiye mbeu yako.

14. Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi mcenje wa madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pace, ndi mwana, namcotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocerera m'cipululu ca Beereseba.

15. Ndipo anatha madzi a m'mcenje ndipo anaika mwana pansi pa citsamba.

16. Ndipo ananka nakhala pansi popenyana naye patari, monga pakugwa mubvi: cifukwa anati, Ndisaone kufa kwa mwana. Ndipo anakhala popenyana naye, nakweza mau ace nalira,

17. Ndipo Mulungu anamva mau a mnyamatayo, ndi mthenga wa Mulungu anamuitana Hagara, ndi mau odzera kumwamba, nati kwa iye, Watani Hagara? usaope; cifukwa Mulungu anamva mau a mnyamata kumene ali.

18. Tauka, nuukitse mnyamatayo, ndi kumgwira m'dzanja lako; cifukwa ndidzamuyesa iye mtundu waukuru.

19. Ndipo Mulungu anamtsegula m'maso mwace, ndipo anaona citsime ca madzi; namuka nadzaza mcenje ndi madzi, nampatsa mnyamata kuti amwe.

20. Ndipo Mulungu anakhala ndi mnyamata, ndipo anakula iye; nakhala m'cipululu, nakhala wauta.

21. Ndipo anakhala m'cipululu ca Parana; ndipo amace anamtengera iye mkazi wa ku dziko la Aigupto.

Werengani mutu wathunthu Genesis 21